Yeremiya 16:11 - Buku Lopatulika11 Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono iwe udzayankhe kuti, ‘Nchifukwa chakuti makolo anu adandisiya Ine,’ akuterotu Chauta. ‘Adatsata milungu ina, namaitumikira ndi kumaipembedza. Adandisiya Ine, ndipo sadamvere malamulo anga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. Onani mutuwo |