Danieli 8:24 - Buku Lopatulika Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Idzakhala yamphamvu kwambiri koma osati mphamvu za iyo yokha. Idzawononga koopsa ndipo idzapambana mu chilichonse chimene idzachite. Mfumuyi idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera omwe. |
Ndipo atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.
Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.
Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza.
Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.
Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nkugwetsa pansi choonadi, ndi kuchita chifuniro chake, ndipo inakula.
Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.
pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.