Danieli 8:10 - Buku Lopatulika10 Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Inakula mpaka inafikira gulu lankhondo la kumwamba, ndipo inagwetsera ena a gulu lankhondolo ndi ena a gulu la nyenyezi ku dziko lapansi ndi kuwapondaponda. Onani mutuwo |
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.