Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.
Danieli 7:5 - Buku Lopatulika Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’ |
Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.
Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.
Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu padziko lonse lapansi.
Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu.
Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.
Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.
Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.