Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 13:8 - Buku Lopatulika

8 Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndidzaŵambwandira ngati chimbalangondo cholandidwa ana. Ndidzathyola nthiti zao, ndipo ndidzaŵamwamwata pomwepo ngati mkango, ndidzaŵankhanthula ngati chilombo choopsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake, ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola. Ndidzawapwepweta ngati mkango; chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:8
11 Mawu Ofanana  

Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya.


Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwake kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.


kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa.


Inu zilombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zilombo inu nonse za m'nkhalango.


Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye.


Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.


Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa