Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.
Danieli 6:25 - Buku Lopatulika Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala pa dziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mfumu Dariyo inalembera anthu a mitundu yonse, ndi anthu a ziyankhulo zosiyanasiyana a mʼdziko lonse kuti, “Mtendere uchuluke pakati panu! |
Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.
Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.
Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana,
Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala padziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu.
mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu.
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.
Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.