Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 7:15 - Buku Lopatulika

15 Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Amakumba mbuna kuti ikhale yozama, koma amagwamo ndiye yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 7:15
19 Mawu Ofanana  

Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu, ndi m'mimba mwao mukonzeratu chinyengo.


Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo.


Indetu, mugwetsera wamasiye msampha, mumkumbira bwenzi lanu mbuna.


Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.


Odzikuza anandikumbira mbuna, ndiwo osasamalira chilamulo chanu.


Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine.


Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.


kuti mumpumitse masiku oipa; kufikira atakumbira woipa mbuna.


Wokumba dzenje adzagwamo, wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa