Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 6:14 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu itamva izi, inavutika kwambiri mu mtima mwake. Iyo inayesa kupeza njira yopulumutsira Danieli. Iyo inachita chotheka chilichonse kufikira kulowa kwa dzuwa kuti imupulumutse.

Onani mutuwo



Danieli 6:14
10 Mawu Ofanana  

Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.


Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahasuwero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; chifukwa chake mfumu siiyenera kuwaleka.


Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya.


Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.


Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.


Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.