Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.
Danieli 5:31 - Buku Lopatulika Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo Dariyo Mmedi analanda ufumuwo ali ndi zaka 62. |
Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.
Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwe, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova.
Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;
Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni;