Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.
Danieli 5:14 - Buku Lopatulika Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera. |
Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.
Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake?
Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.
Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti,
Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?
Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi.
Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.