Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya.
Danieli 5:10 - Buku Lopatulika Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike! |
Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya.
Potero munditonthozeranji nazo zopanda pake, popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha?
Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake.
Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.
Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire.