Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 5:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike!

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;

Onani mutuwo Koperani




Danieli 5:10
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”


Koma inu mukundipaka mabodza; nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!


“Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”


Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”


Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali!


Nkhope yake inasandulika ndipo inachita mantha, nkhongono zii, mawondo gwedegwede.


Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali!


Choncho akalonga ndi nduna pamodzi anapita kwa mfumu ndipo anati: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo wautali!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa