Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 4:21 - Buku Lopatulika

umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama zakuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

mtengo umene masamba ake anali okongola ndiponso unali ndi zipatso zochuluka zokwanira kudya anthu onse a dziko lapansi. Mtengowu unkapereka mthunzi ku zirombo zonse zakuthengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinayika zisa pa nthambi zake.

Onani mutuwo



Danieli 4:21
8 Mawu Ofanana  

m'mwemo mbalame zimanga zisa zao; pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza.


paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.


Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse zakuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.


ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.


Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi.


Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera padziko lonse lapansi,


ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.


Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.