Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 4:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 mtengo umene masamba ake anali okongola ndiponso unali ndi zipatso zochuluka zokwanira kudya anthu onse a dziko lapansi. Mtengowu unkapereka mthunzi ku zirombo zonse zakuthengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinayika zisa pa nthambi zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama zakuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:21
8 Mawu Ofanana  

Mbalame zimamanga zisa zawo; kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.


Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake.


Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.


Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.


Mtengowo unakula ndi kulimba ndipo msonga yake inafika mpaka mlengalenga; umaonekera pa dziko lonse lapansi.


Mtengo munawuona uja, umene unkakulirakulira kwambiri ndi kulimba, ndi msonga yake inafika mlengalenga, ndi kuonekera ku dziko lonse lapansi,


Inu mfumu, ndinu mtengo umenewo! Inu mwakhala wamkulu ndi wamphamvu; ukulu wanu wakula mpaka wakhudza mlengalenga, ndipo ufumu wanu wafika mpaka ku malo akutali a dziko lapansi.


Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa