Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
Danieli 2:7 - Buku Lopatulika Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.” |
Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake.
Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti chinthuchi chandichokera.
Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe.
Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.