Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 11:26 - Buku Lopatulika

Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amene amadya chakudya ndi mfumu adzamuukira; gulu lake lankhondo lidzagonjetsedwa, ndipo ambiri adzafera ku nkhondo.

Onani mutuwo



Danieli 11:26
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anachoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wake; ameneyo ananena naye, Anakuuza chiyani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzachira ndithu.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo aakulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake.


Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano.


Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.


Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine.


Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m'mbale.


Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.