Danieli 10:20 - Buku Lopatulika Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera. |
Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.
Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.
Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.
Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.
Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.