Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu.
Danieli 1:11 - Buku Lopatulika Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Danieli anati kwa kapitawo amene anali mkulu wa nduna za mfumu amene anamuyika kuti ayangʼanire Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya, |
Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu.
Pamenepo kapitaoyo anachotsa chakudya chao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka.
Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi;