Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.
Danieli 1:1 - Buku Lopatulika Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo. |
Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.
Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.
Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.
Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,
Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala mu Yerusalemu.
Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,
Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,
Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:
Amenewa ndi anthu amene Nebukadinezara anatenga ndende: chaka chachisanu ndi chiwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;
Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?