Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 45:1 - Buku Lopatulika

1 Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Naŵa mau amene mneneri Yeremiya adalembetsa Baruki mwana wa Neriya m'buku, chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Uwu ndi uthenga umene mneneri Yeremiya anawuza Baruki mwana wa Neriya mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa mwana ya Yosiya kuti alembe mʼbuku.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 45:1
18 Mawu Ofanana  

Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;


Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti,


ndipo ndinapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata yogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo nditapereka kalata yogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,


Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,


Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.


Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.


Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:


Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pamtsinje wa Yufurate mu Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.


Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake.


Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa