Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:12 - Buku Lopatulika

12 Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi wa aphungu ake, adadza ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:12
16 Mawu Ofanana  

Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.


Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.


Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu,


Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba ino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.


Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.


Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti,


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake.


chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera mu Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;


Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo.


Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa