Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
Amosi 3:3 - Buku Lopatulika Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kodi anthu aŵiri nkuyendera pamodzi, osapangana? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi asanapangane? |
Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.
Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a padziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse.
Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu?
Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.