Amosi 4:1 - Buku Lopatulika1 Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Mverani mau aŵa akazi inu okhala ku Samariya amene mukungonenepa ngati ng'ombe za m'dera la Basani, inu amene mumavutitsa osauka ndi kuzunza osoŵa. Ntchito nkumangolamula amuna anu kuti, “Tipatseni zoziziritsa kukhosi.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya, inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!” Onani mutuwo |