Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 3:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndidzagwetseratu nyumba za nthaŵi yachisanu ndi za nthaŵi yamafundi. Nyumba zaminyanga zidzaonongeka, ndithu nyumba zazikulu zidzaphwasuka.” Akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha; nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:15
10 Mawu Ofanana  

Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi mizinda yonse adaimanga, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.


M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo.


Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yachisanu mwezi wachisanu ndi chinai; ndipo munali moto m'mbaula pamaso pake.


koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.


Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake padziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing'ono ichite mindala.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa