Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.
Akolose 1:8 - Buku Lopatulika amenenso anatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amenenso anatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye amene adatidziŵitsa za chikondi chomwe Mzimu Woyera adaika mwa inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani. |
Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse;
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;