Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:22 - Buku Lopatulika

22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzaonekera poyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera.

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:22
10 Mawu Ofanana  

Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.


Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala choonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kuvumbuluka.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa