Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.
Ahebri 3:3 - Buku Lopatulika Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu womanga nyumba amalandira ulemu woposa ulemerero wa nyumbayo. Momwemonso Yesu ngwoyenera kulandira ulemerero woposa ulemerero wa Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. |
Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:
Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.
Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.
koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.