Afilipi 4:2 - Buku Lopatulika Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. |
Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.
ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: