Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.
Afilipi 2:24 - Buku Lopatulika koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa. |
Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.
Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.
Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.