Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.
Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.
Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Mowabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleke.
Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka.
Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu.
Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.