Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 8:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa:

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina amene adaŵagonjetsa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:11
8 Mawu Ofanana  

anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.


Pamene ntchito yonse imene Mfumu Solomoni inagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka: siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Yehova.


Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.


Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka.


Pamene ntchito yonse imene Solomoni anagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka; siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.


“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa