Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
2 Samueli 7:28 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munalonjezana ndi mnyamata wanu kumchitira chabwino ichi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munalonjezana ndi mnyamata wanu kumchitira chabwino ichi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo tsopano Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu, ndipo mau anu ngoona. Mwalonjeza kuti mudzandichitira zabwino zotere ine mtumiki wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. |
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;