Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
2 Samueli 5:22 - Buku Lopatulika Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi ina Afilisti adabweranso, nandanda m'chigwa chija cha Refaimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu; |
Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.
Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.
Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.
nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.