ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti.
2 Samueli 3:7 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa, mwana wa Aya. Tsono Isiboseti adafunsa Abinere kuti, “Chifukwa chiyani wakaloŵa kwa mzikazi wa bambo wanga?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?” |
ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomoni, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga.