2 Samueli 3:37 - Buku Lopatulika Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumire kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumira kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho onse amene ankakhala ndi mfumu pamodzi ndi Aisraele onse adamvetsa tsiku limenelo kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abinere mwana wa Nere aphedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe. |
Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.
Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.
wa hafu la fuko la Manase mu Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere;
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.