Pamene anafika iwo pamwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka.
2 Samueli 3:30 - Buku Lopatulika Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Yowabu ndi mbale wake Abisai adapha Abinere chifukwa choti Abinereyo anali ataŵaphera mbale wao Asahele pa nkhondo ya ku Gibiyoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni). |
Pamene anafika iwo pamwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka.
Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.