2 Samueli 20:8 - Buku Lopatulika8 Pamene anafika iwo pamwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pamene anafika iwo pa mwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Nthaŵi imene adafika ku mwala waukulu umene uli ku Gibiyoni, Amasa adabwera kudzakumana nawo. Tsono Yowabu adaavala malaya ankhondo, ndipo pamwamba pa malayawo m'chiwuno mwake, panali lamba womangirirapo lupanga lam'chimake. Pamene ankayenda, lidasololoka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake. Onani mutuwo |