Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
2 Samueli 3:15 - Buku Lopatulika Pomwepo Isiboseti anatumiza namchotsera kwa mwamuna wake, kwa Palatiele mwana wa Laisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Isiboseti anatumiza namchotsera kwa mwamuna wake, kwa Palatiele mwana wa Laisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Isiboseti adatuma anthu kuti akamtenge Mikalayo kwa mwamuna wake Palatiele, mwana wa Laisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi. |
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.
Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.
Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu.