Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
2 Samueli 3:13 - Buku Lopatulika Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adati, “Chabwino, tipangana. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: sudzandiwona ukapanda kubwera ndi Mikala, mwana wamkazi wa Saulo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.” |
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga.
Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.
Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.
Ndipo polowa likasa la chipangano la Yehova m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo anasuzumira pazenera, nao mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwake.