2 Samueli 24:19 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva mau a Gadiwo, Davide adapita monga momwe Chauta adaalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anapita monga momwe Yehova anamulamulira kudzera mwa Gadi. |
Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.
Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.
Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.
koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.