Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 24:11 - Buku Lopatulika

Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Davide atadzuka m'maŵa, Chauta adalankhula ndi Gadi, mneneri wa Davide, namuuza kuti,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Davide asanadzuke mmawa mwake mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlosi wa Davide kuti,

Onani mutuwo



2 Samueli 24:11
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.


Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho.


Namwalira Azuba, ndi Kalebe anadzitengera Efurata, amene anambalira Huri.


Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti,


awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yake. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna khumi ndi anai, ndi ana aakazi atatu.


Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;


Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.


Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; chokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.


Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale.