1 Samueli 9:9 - Buku Lopatulika9 Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Kale m'Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 (Kale ku Israele, munthu akamapita kukapempha nzeru kwa Mulungu, ankati, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene tsopano amamutchula mneneri, kale ankatchulidwa mlosi). Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 (Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi). Onani mutuwo |
Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.