Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.
2 Samueli 23:11 - Buku Lopatulika Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wotsatana ndi ameneyo anali Sama, mwana wa Age Muharari. Nthaŵi ina Afilisti adasonkhana ku Lehi kumene kunali munda wa mphodza. Aisraele nkuthaŵa Afilisti aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo. |
Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.