Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;
2 Samueli 21:19 - Buku Lopatulika Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka nkhondo inanso idabuka ndi Afilisti omwewo ku Gobu. Tsono Elihanani, mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu, adapha Lahimi, mbale wa Goliyati wa ku Gati uja, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu. |
Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;
Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliyati Mgiti, amene luti la mkondo wake linanga mtanda woombera nsalu.
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.