Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
2 Samueli 20:12 - Buku Lopatulika Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monsemo nkuti Amasa atagona pa mseu ndi kuvimvinizika m'magazi ake. Ndipo aliyense amene ankabwera, ankati akamuona, nkuima. Tsono munthu wa Yowabu uja ataona kuti anthu akuima, adanyamula Amasa uja, kumchotsa mumseumo, nakamuika ku thengo, nkumfunditsa chovala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. |
Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m'mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.
Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.
Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.