Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.
2 Samueli 2:27 - Buku Lopatulika Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu adayankha kuti, “Ndithudi, ndikulumbira, pali Mulungu wamoyo, ukadapanda kulankhula, ankhondo angaŵa sakadaleka kuŵathamangitsa abale aowo mpaka maŵa m'maŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, ukanapanda kuyankhula, ankhondo anga akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mmawa.” |
Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.
Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?
Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso.
Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine, ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,
Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.
Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.
Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.