Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide.
2 Samueli 2:14 - Buku Lopatulika Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abinere adauza Yowabu kuti, “Anyamata anu ndi athu abwere, amenyane tiwone.” Yowabu adati, “Chabwino, namenyane.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abineri anati kwa Yowabu, “Tiye tibweretse ena mwa anyamata athu kuti amenyane patsogolo pathupa.” Yowabu anayankha, “Chabwino, amenyane.” |
Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide.
Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.
Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abinere ndi anthu a Israele anathawa pamaso pa anyamata a Davide.
Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.
Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.
Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.