Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.
2 Samueli 2:11 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Davide adakhala mfumu ya fuko la Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi. |
Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.
Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu zitatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.
Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu mu Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu mu Yerusalemu.
Anambadwira asanu ndi mmodzi mu Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi mu Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.