Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.
2 Samueli 2:10 - Buku Lopatulika Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide. |
Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.
Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.