Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:10
4 Mawu Ofanana  

Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.


Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu.


Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense.


Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa